Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 2:16 - Buku Lopatulika

16 koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Koma adadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama yosalankhula, adalankhula ngati munthu, kuletsa zamisala za mneneriyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo.

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 2:16
8 Mawu Ofanana  

Pamene mulanga munthu ndi zomdzudzula chifukwa cha mphulupulu, mukanganula kukongola kwake monga mumachita ndi njenjete. Indedi, munthu aliyense ali chabe.


Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;


Ichi ndi choipa m'zonse zichitidwa pansi pano, chakuti kanthu kamodzi kagwera onse; indetu, mtimanso wa ana a anthu wadzala udyo, ndipo misala ili m'mtima wao akali ndi moyo, ndi pamenepo apita kwa akufa.


Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israele adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, chifukwa cha kuchuluka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukulu.


Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona?


Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa