Numeri 22:27 - Buku Lopatulika Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo bulu wake anaona mthenga wa Yehova, nagona pansi, Balamu ali pamsana pake; ndipo Balamu adapsa mtima, nampanda bulu ndi ndodo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adagona pansi, Balamu ali pamsana pake. Balamu adapsa mtima kwambiri, namenya buluyo ndi ndodo yake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anagona pansi Balaamu ali pa msana, ndipo iye anakwiya ndi kumumenya ndi ndodo yake. |
Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima.