Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.
Numeri 22:25 - Buku Lopatulika Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Buluyo ataona mngelo wa Chauta, adadzipanikiza ku khoma, nakanikiza phazi la Balamu kukhomako. Pomwepo Balamu adamenya buluyo kachiŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Bulu uja ataona mngelo wa Yehova anadzipanikiza ku khoma, kukhukhuza phazi la Balaamu kukhomako. Ndipo pomwepo Balaamu anamenya buluyo kachiwiri. |
Taima tsopano ndi maphendo ako, ndi unyinji wa matsenga ako, m'menemo iwe unagwira ntchito chiyambire ubwana wako; kuti kapena udzatha kupindula, kuti kapena udzapambana.
Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga.
Pamenepo mthenga wa Yehova anapitiriranso, naima popapatiza, popanda popatukira kulamanja kapena kulamanzere.