Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.
Numeri 22:24 - Buku Lopatulika Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo mthenga wa Yehova anaima m'njira yopapatiza ya minda yampesa; mbali ina kuli linga, mbali ina linga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pambuyo pake mngelo wa Chauta uja adakaimirira m'kanjira kophaphatiza, kodzera pakati pa minda yamphesa, kokhala ndi khoma pa mbali zonse ziŵiri. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka mngelo wa Yehova anayima mʼkanjira kakangʼono pakati pa minda iwiri ya mpesa yokhala ndi makoma mbali zonse |
Ndipo buluyo anaona mthenga wa Yehova alikuima m'njira, ndi lupanga lake ku dzanja lake; ndi bulu anapatuka m'njira, nalowa kuthengo; ndipo Balamu anampanda bulu kumbwezera kunjira.
Ndipo bulu anaona mthenga wa Yehova, nadzikankhira kulinga, nakanikiza phazi la Balamu kulinga; ndipo anampandanso.