Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.
Numeri 22:21 - Buku Lopatulika Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga bulu wake, namuka nao akalonga a ku Mowabu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Balamu anauka m'mawa namanga bulu wake, namuka nao akalonga a ku Mowabu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Balamu, atadzuka m'maŵa mwake, adaika chishalo pa bulu wake, ndipo adanyamuka pamodzi ndi akalonga aja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Balaamu anadzuka mmawa, namanga bulu wake wamkazi ndipo anapita ndi akuluakulu a Mowabu. |
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa namanga bulu wake, natengako anyamata ake awiri pamodzi naye, ndi Isaki mwana wake, nawaza nkhuni za nsembe yopsereza, nauka, nanka kumalo komwe Mulungu anamuuza iye.
posiya njira yolunjika, anasokera, atatsata njira ya Balamu mwana wa Beori, amene anakonda mphotho ya chosalungama;
koma anadzudzulidwa pa kulakwa kwake mwini; bulu wopanda mau, wolankhula ndi mau a munthu, analetsa kuyaluka kwa mneneriyo.