Ndipo Balamu anauka m'mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu.
Numeri 22:14 - Buku Lopatulika Pamenepo akalonga a Mowabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati Alikukana Balamu kudza nafe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo akalonga a Mowabu ananyamuka, nafika kwa Balaki, nati Alikukana Balamu kudza nafe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono akalonga a Mowabu aja adanyamuka napita kwa Balaki, ndipo adakamuuza kuti, “Balamu wakana kubwera.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kotero akuluakulu a Mowabu anabwerera kwa Balaki ndi kukanena kuti, “Balaamu wakana kubwera nafe.” |
Ndipo Balamu anauka m'mawa, nati kwa akalonga a Balaki, Mukani ku dziko lanu; popeza Yehova andikaniza kuti ndisapite nanu.
Ndipo Balaki anati kwa Balamu, Kodi sindinatumize kwa iwe ndithu kukakuitana? Unalekeranji kudza kwa ine? Sindikhoza kodi kukuchitira ulemu?