Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.
Numeri 21:22 - Buku Lopatulika Ndipitire pakati padziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipitire pakati pa dziko lako; sitidzapatuka kulowa m'munda, kapena m'munda wampesa, sitidzamwako madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu, kufikira tapitirira malire ako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Mutilole kuti tidzere m'dziko mwanumo. Sitidzadzera m'minda mwanu, kapena m'mipesa mwanu. Sitidzamwa madzi a m'chitsime chanu. Tidzangotsata mseu wanu waukulu mpaka titadutsa dziko lanulo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tiloleni kuti tidutse mʼdziko mwanu. Sitidzapatukira mʼminda mwanu kapena mu mpesa wanu kapena kumwa madzi mʼchitsime chili chonse. Tidzayenda mu msewu waukulu wa mfumu mpaka titadutsa malire a dziko lanu.” |
Pamenepo tinafuulira kwa Yehova, ndipo anamva mau athu, natuma mthenga, natitulutsa mu Ejipito; ndipo, taonani, tili mu Kadesi, ndiwo mzinda wa malekezero a malire anu.
Tipitetu pakati padziko lanu; sitidzapitira pamunda, kapena munda wampesa, sitidzamwa madzi a m'zitsime; tidzatsata mseu wachifumu; sitidzapatukira kulamanja kapena kulamanzere, mpaka titapitirira malire anu.