Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Numeri 2:31 - Buku Lopatulika Owerengedwa onse a chigono cha Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Owerengedwa onse a chigono cha Dani ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu kudza zisanu ndi ziwiri mphambu mazana asanu ndi limodzi. Iwo ndiwo aziyenda m'mbuyo paulendo, monga mwa mbendera zao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chiŵerengero chathunthu cha anthu a m'zithando za Dani ndi 157,600. Iwo akhale a gulu lotsiriza poyenda motsatira mbendera zao.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu onse aamuna mu msasa wa Dani chiwerengero chawo ndi 157,600. Iwo azidzanyamuka pomaliza, ndi mbendera zawo. |
Pamenepo anayenda a mbendera ya chigono cha ana a Dani, ndiwo a m'mbuyombuyo a zigono zonse, monga mwa magulu ao; ndi pa gulu lake anayang'anira Ahiyezere mwana wa Amisadai.
Owerengedwa onse a chigono cha Rubeni ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi chimodzi kudza mazana anai mphambu makumi asanu, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsatana nao otsogolerawo.
Owerengedwa onse a chigono cha Efuremu ndiwo zikwi makumi khumi mphambu zisanu ndi zitatu kudza zana limodzi, monga mwa makamu ao. Iwo ndiwo aziyenda gulu lachitatu paulendo.
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zitatu kudza mazana anai.
Owerengedwa onse a chigono cha Yuda ndiwo zikwi makumi khumi mphambu makumi asanu ndi atatu kudza zisanu ndi chimodzi mphambu mazana anai, monga mwa makamu ao. Ndiwo azitsogolera ulendo.