nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
Numeri 17:4 - Buku Lopatulika Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndodozo uziike m'chihema chamsonkhano patsogolo pa bokosi laumboni pamene ndimakumana nawe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe. |
nupere china chisalale, nuchiike chakuno cha mboni m'chihema chokomanako, kumene ndidzakomana ndi iwe; uchiyese chopatulika ndithu.
Nuliike chakuno cha nsalu yotchinga ili ku likasa la mboni, patsogolo pa chotetezerapo chili pamwamba pa mboni, pomwe ndidzakomana ndi iwe.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Bweza ndodo ya Aroni kuiika chakuno cha mboni, isungike ikhale chizindikiro cha pa ana opikisana; kuti unditsirizire madandaulo ao, kuti ungafe.
Ndipo ulembe dzina la Aroni pa ndodo ya Levi; pakuti pakhale ndodo imodzi pa mkulu yense wa nyumba za makolo ao.