Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 17:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Uyike ndodozo mu tenti ya msonkhano, kutsogolo kwa Bokosi la Umboni, kumene ndimakumana nawe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo uziike m'chihema chokomanako, chakuno cha mboni, kumene ndikomana ndi inu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Tsono ndodozo uziike m'chihema chamsonkhano patsogolo pa bokosi laumboni pamene ndimakumana nawe.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 17:4
7 Mawu Ofanana  

Upere gawo lina mosalala kwambiri ndipo utapepo pangʼono ndi kuyika patsogolo pa Bokosi la Chipangano mu tenti ya msonkhano, kumene ine ndidzakumane nawe. Lubani ameneyu kwa inu adzakhala wopatulika kwambiri.


Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe.


Yehova anawuza Mose kuti, “Bwezera ndodo ya Aaroni patsogolo pa Bokosi la Umboni, kuti chikhale chizindikiro cha kuwukira kwawo. Zimenezi zidzathetsa kudandaula kwawo kotsutsana nane, kuopa kuti angafe.”


Pa ndodo ya Levi ulembepo dzina la Aaroni, chifukwa pafunika ndodo imodzi ya mtsogoleri pa fuko lililonse.


Mose anayika ndodozo pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa