Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana.
Numeri 16:31 - Buku Lopatulika Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang'ambika pansi pao; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo kunali, pakutha iye kunena mau awa onse, nthaka inang'ambika pansi pao; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose atangomaliza kulankhula mau ameneŵa, nthaka idang'ambika pamene padaali iwopo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atangotsiriza kuyankhula zimenezi, nthaka ya pamene anayimapo inagawikana |
Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi lili kugwedezeka kopambana.
Koma Yehova akalenga chinthu chatsopano, ndi nthaka ikayasama pakamwa pake, nikawameza ndi zonse ali nazo, nakatsikira iwo kumanda ali ndi moyo; pamenepo mudzadziwa kuti anthu awa anyoza Mulungu.
ndi dziko linayasama pakamwa pake ndi kuwameza, iwo ndi mabanja ao, ndi amuna ao onse akutsata Kora, ndi akatundu ao onse.
Ndipo anthu anatsutsana ndi Mose, nanena, nati, Mwenzi titangomwalira muja abale athu anamwalira pamaso pa Yehova!
Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.
ndi chimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pake, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israele wonse.
Tsoka kwa iwo! Pakuti anayenda m'njira ya Kaini, ndipo anadziononga m'chisokero cha Balamu chifukwa cha kulipira, natayika m'chitsutsano cha Kora.