Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 16:2 - Buku Lopatulika

ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo anauka pamaso pa Mose, pamodzi ndi amuna mazana awiri mphambu makumi asanu a ana a Israele, ndiwo akalonga a khamulo, oitanidwa a msonkhano, amuna omveka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

adakopa anthu. Adaukira Mose, iwowo pamodzi ndi atsogoleri a Aisraele 250, osankhidwa ndi anthu pa msonkhano, anthu otchuka.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

ndipo anawukira Mose. Mʼgulu mwawo munali atsogoleri a Aisraeli 250, anthu otchuka amene anasankhidwa ndi anthu pa msonkhano.

Onani mutuwo



Numeri 16:2
10 Mawu Ofanana  

Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.


Ndi a ana a Efuremu zikwi makumi awiri mphambu mazana asanu ndi atatu, ngwazi zamphamvu, anthu omveka m'nyumba za makolo ao.


Ndipo akulu a nyumba za makolo ao ndi awa: Efere, ndi Isi, ndi Eliyele, ndi Aziriele, ndi Yeremiya, ndi Hodaviya, ndi Yadiyele, anthu amphamvu ndithu, anthu omveka, akulu a nyumba za makolo ao.


Ndi mbiri yako inabuka mwa amitundu chifukwa cha kukongola kwako; pakuti ndiko kwangwiro, mwa ulemerero wanga ndinauika pa iwe, ati Ambuye Yehova.


Iwowa anavula umaliseche wake, anatenga ana ake aamuna ndi aakazi, namupha iyeyu ndi lupanga; ndi dzina lake linamveka mwa akazi atamchitira maweruzo.


Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mafuko a makolo ao; ndiwo akulu a zikwizo za Israele.


Ndipo Miriyamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adamtenga; popeza adatenga mkazi Mkusi.


Ndipo moto unatuluka kwa Yehova, ndi kunyeketsa amuna mazana awiri ndi makumi asanu aja akubwera nacho chofukiza.


Ndi ana a Eliyabu: Nemuwele, ndi Datani ndi Abiramu. Iwo ndiwo Datani ndi Abiramu omwe aja oitanidwa a khamu, amene anatsutsana ndi Mose ndi Aroni mu msonkhano wa Kora, muja anatsutsana ndi Yehova;


Atate wathu adamwalira m'chipululu, ndipo sanakhale iye pakati pa msonkhano wa iwo akusonkhana kutsutsana ndi Yehova, mu msonkhano wa Kora; koma anafera zoipa zakezake; ndipo analibe ana aamuna.