Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Numeri 16:18 - Buku Lopatulika

Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo la chihema chokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Potero munthu yense anatenga mbale yake yofukizamo, naikamo moto, naikapo chofukiza, naima pa khomo la chihema chokomanako pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Choncho munthu aliyense adatenga chofukizira lubani, naikamo moto, ndi kuthiramo lubani, ndipo adakaimirira pa chipata cha chihema chamsonkhano, pamodzi ndi Mose ndi Aroni.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho munthu aliyense anatenga chofukizira chake nayikamo moto ndi lubani, ndipo anayima pamodzi ndi Mose ndi Aaroni pa khomo la tenti ya msonkhano.

Onani mutuwo



Numeri 16:18
7 Mawu Ofanana  

Koma atakhala wamphamvu, mtima wake unakwezeka momuononga, nalakwira Yehova Mulungu wake; popeza analowa mu Kachisi wa Yehova kufukiza paguwa la nsembe la chofukiza.


natenge mbale ya zofukiza yodzala ndi makala amoto, kuwachotsa paguwa la nsembe, pamaso pa Yehova, ndi manja ake odzala ndi chofukiza chopera cha fungo lokoma, nalowe nayo m'tseri mwa nsalu yotchinga;


naike chofukizacho pamoto pamaso pa Yehova, kuti mtambo wa chofukiza chiphimbe chotetezerapo chokhala pamboni, kuti angafe.


nimutenge munthu yense mbale yake yofukizamo, nimuike chofukiza m'mwemo, nimubwere nazo, yense mbale yake yofukizamo pamaso pa Yehova, mbale zofukizamo mazana awiri ndi makumi asanu; ndi iwe, ndi Aroni, yense mbale yake yofukizamo.


Ndipo Kora anasonkhanitsa khamu lonse mopikisana nao ku khomo la chihema chokomanako; ndipo ulemerero wa Yehova unaoneka kwa khamu lonse.


Nena ndi Eleazara mwana wa Aroni wansembe, kuti aphule mbale zofukiza pakati pa moto, nutaye makalawo uko kutali: pakuti zili zopatulika;


Ndipo anaima pakati pa akufa ndi amoyo; ndi mliri unaleka.