Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.
Numeri 16:12 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako: Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatuma kukaitaniza Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu; koma anati, Sitifikako: Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Mose adatuma munthu kukaitana Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu. Ndipo iwo adati, “Ife sitibwera kumeneko. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Mose anayitana Datani ndi Abiramu, ana aamuna a Eliabu koma iwo anati, “Sitibwera! |
Munthu wanzeru akatsutsana ndi munthu wopusa, ngakhale akwiya, ngakhale aseka, palibe mtendere.
Ndi anthu adzavutidwa, yense ndi wina, yense ndi mnansi wake; mwana adzadzinyaditsa yekha pa akulu, ndi onyozeka pa olemekezedwa.
Koma Kora, mwana wa Izihara, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, anatenga Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, ndi Oni mwana wa Peleti, ana a Rubeni;
Chifukwa chake, iwe ndi khamu lonse mwasonkhana kutsutsana ndi Yehova; ndipo Aroniyo ndani, kuti mudandaule pa iye?
kodi ndi chinthu chaching'ono kuti watikweza kutichotsa m'dziko moyenda mkaka ndi uchi ngati madzi, kutipha m'chipululu; koma udziyesanso ndithu kalonga wa ife?
Momwemonso iwo m'kulota kwao adetsa matupi ao, napeputsa ufumu, nachitira mwano maulemerero.