Numeri 15:23 - Buku Lopatulika ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova analamula, ndi kunkabe m'mibadwo yanu; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndizo zonse Yehova anakuuzani ndi dzanja la Mose, kuyambira tsikulo Yehova anauza, ndi kunkabe m'mibadwo yanu; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa ndi zonse zimene adakulamulani kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Chauta adapereka lamulo mpaka m'tsogolo mwake pa mibadwo yanu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, |
pamenepo kudzali, ngati anachichita osati dala, osachidziwa khamulo, khamu lonse lipereke ng'ombe yamphongo ikhale nsembe yopsereza, ya fungo lokoma ya Yehova, pamodzi ndi nsembe yake yaufa, ndi nsembe yake yothira, monga mwa chiweruzo chake; ndi tonde mmodzi akhale nsembe yauchimo.