Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;
Numeri 15:2 - Buku Lopatulika Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mukakalowa m'dziko lokakhalamo inu, limene ndilikupatsa inu, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mukakalowa m'dziko lokakhalamo inu, limene ndilikupatsa inu, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Uza Aisraele kuti, ‘Mukadzaloŵa m'dziko limene ndidzakupatsenilo, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo, |
Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, ndi kucheka dzinthu zake, pamenepo muzidza nao mtolo wa zipatso zoyamba za masika anu kwa wansembe;
Nena ndi ana a Israele, nuti nao, Mutakalowa m'dziko limene ndikupatsani, dzikoli lizisungira Yehova Sabata.
Awa ndi malemba ndi maweruzo, muziwasamalirawa kuwachita m'dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu anakupatsani likhale lanulanu, masiku onse akukhala ndi moyo inu padziko lapansi.
pakuti mpaka lero simunafikire mpumulo ndi cholowa, zimene Yehova Mulungu wanu adzakupatsani.