Numeri 11:9 - Buku Lopatulika Ndipo pakugwa mame pachigono usiku, mana anagwapo. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pakugwa mame pachigono usiku, mana anagwapo. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamene mame ankagwa usiku pamahemapo, ankagwera kumodzi ndi mana. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mame akamagwa pa msasawo usiku ankagwera kumodzi ndi manawo. |
Ndipo Mose anamva anthu alikulira m'mabanja ao, yense pakhomo pa hema wake; ndipo Yehova anapsa mtima ndithu, ndipo kudamuipira Mose.
Anthu amanka, nawaola, nawapera ndi mphero, kapena kuwasinja mumtondo, nawaphika m'mphika, nawaumba timitanda; ndi powalawa anali ngati timitanda tokazinga ndi mafuta.
Chiphunzitso changa chikhale ngati mvula; maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.