Numeri 11:32 - Buku Lopatulika Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anthu anauka tsiku lonselo, ndi usiku wake wonse, ndi mawa lake lonse, nakusa zinzirizo; wokusa pang'ono anakusa zodzaza mahomeri khumi; ndipo anadziyanikira izi pozungulira pa chigono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu atadzuka, ankagwira zinzirizo masana onse ndi usiku. M'maŵa mwakenso tsiku lathunthu, adachita chimodzimodzi. Panalibe ndi mmodzi yemwe amene adagwira zinziri zochepera makilogaramu chikwi chimodzi. Ndipo adaziyanika kuzungulira mahema onsewo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsiku limenelo masana onse mpaka usiku ndiponso tsiku lotsatiralo, anthu anatuluka kunja kukatola zinziri. Palibe amene anasonkhanitsa zochepera makilogalamu 1,000 ndipo anaziyanika kuzungulira msasa wonse. |
Efa ndi bati zikhale za muyeso umodzi, bati liyese limodzi la magawo khumi la homeri, efa lomwe liyese limodzi la magawo khumi la homeri; muyeso wao uyesedwa monga mwa homeri.
Nyamayi ikali pakati pa mano, asanaitafune, Mulungu anapsa mtima pa anthuwa, ndipo Yehova anawakantha anthu ndi kukantha kwakukulu ndithu.