Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!
Numeri 11:30 - Buku Lopatulika Ndipo Mose ndi akulu onse a Israele anasonkhana kuchigono. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose ndi akulu onse a Israele anasonkhana kuchigono. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Mose ndi atsogoleri a Aisraele aja adabwerera ku mahema. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose ndi akuluakulu a Israeli aja anabwerera ku msasa. |
Koma Mose anati kwa iye, Kodi uchita nsanje nao chifukwa cha ine? Mwenzi anthu onse a Yehova atakhala aneneri? Mwenzi Yehova atawaikira mzimu wake!
Ndipo kudachokera mphepo kwa Yehova, n'kudza nazo zinziri zochokera kunyanja, ndipo zidagwa kuchigono, ulendo wa tsiku limodzi dera lino, ndi ulendo wa tsiku limodzi dera lina, pozungulira pa chigono, ndipo zinabisa nthaka ngati muyeso wa mikono iwiri.