Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Numeri 11:24 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anatuluka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akulu a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa chihema. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anatuluka, nauza anthu mau a Yehova; nasonkhanitsa akulu a anthu makumi asanu ndi awiri, nawaimika pozungulira pa chihema. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Choncho Mose adatuluka nakauza anthu mau a Chauta aja. Adasonkhanitsa anthu makumi asanu ndi aŵiri mwa akuluakulu a Aisraele, naŵakhazika mozungulira chihema chamsonkhano. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Choncho Mose anatuluka nakawuza anthu zomwe Yehova ananena. Anasonkhanitsa pamodzi akuluakulu makumi asanu ndi awiri aja ndi kuwayimiritsa mozungulira Chihema. |
Ndipo anamuingitsa munthuyo; nakhazika akerubi cha kum'mawa kwake kwa munda wa Edeni, ndi lupanga lamoto lakuzungulira ponsepo, lakusunga njira ya ku mtengo wa moyo.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Undisonkhanitsire amuna makumi asanu ndi awiri mwa akulu a Israele, amene uwadziwa kuti ndiwo akulu a anthu, ndi akapitao ao; nubwere nao ku chihema chokomanako, kuti aimeko pamodzi ndi iwe.
Koma amuna awiri anatsalira m'chigono, dzina la wina ndiye Elidadi, dzina la mnzake ndiye Medadi; ndipo mzimuwo unakhala pa iwo; iwo ndiwo mwa oitanidwawo, koma sanatuluke kunka kuchihema; ndipo ananenera m'chigono.