Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.
Numeri 10:8 - Buku Lopatulika Ana aamuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ana amuna a Aroni, ansembe, ndiwo aziliza malipenga; ndipo akhale kwa inu lemba losatha ku mibadwo yanu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ana a Aroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipenga. Ntchito ya malipengayi ndi lamulo lamuyaya pa mibadwo yanu yonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ana a Aaroni, ansembe aja, ndiwo aziliza malipengawo. Zimenezi zikhale zokhazikika kwa inu ndi ku mibado yanu yonse. |
Ndi Sebaniya, ndi Yosafati, ndi Netanele, ndi Amasai, ndi Zekariya, ndi Benaya, ndi Eliyezere, ansembe, analiza malipenga ku likasa la Mulungu; ndi Obededomu ndi Yehiya anali odikira a likasa.
ndi Benaya ndi Yahaziele ansembe ndi malipenga kosalekeza, ku likasa la chipangano la Mulungu.
Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.