Numeri 1:49 - Buku Lopatulika Fuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israele; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Fuko la Levi lokha usaliwerenge, kapena kuona kufikira kwao mwa ana a Israele; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Fuko la Levi usaliŵerenge ai, anthu ake usaŵalembere kumodzi ndi Aisraele enawo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Usawerenge fuko la Levi kapena kuliphatikiza mʼkawundula wa Aisraeli. |
Ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi awiri mphambu zitatu, mwamuna yense wa mwezi umodzi ndi mphambu; popeza sanawerengedwe pakati pa ana a Israele; chifukwa sanawapatse cholowa mwa ana a Israele.