ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;
Numeri 1:37 - Buku Lopatulika owerengedwa ao a fuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 owerengedwa ao a fuko la Benjamini, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Benjamini, adapezeka kuti ali 35,400. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Benjamini chinali 35,400. |
ndi a Benjamini: Eliyada ngwazi yamphamvu, ndi pamodzi ndi iye zikwi mazana awiri ogwira mauta ndi zikopa;
A ana a Benjamini, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
A ana a Dani, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi atatu mphambu zisanu kudza mazana anai.
Iwo ndiwo ana a Benjamini monga mwa mabanja ao; ndipo owerengedwa ao ndiwo zikwi makumi anai mphambu zisanu kudza mazana asanu ndi limodzi.
Ndipo anawerenga ana a Benjamini a m'mizinda tsiku lija amuna zikwi makumi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi akusolola lupanga; osawerenga okhala mu Gibea, ndiwo amuna osankhika mazana asanu ndi awiri.