A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Numeri 1:31 - Buku Lopatulika owerengedwa ao a fuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 owerengedwa ao a fuko la Zebuloni, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Zebuloni, adapezeka kuti ali 57,400. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Zebuloni chinali 57,400. |
A ana a Zebuloni, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
A ana a Yosefe, ndiwo a ana a Efuremu, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Ndi khamu lake, ndi owerengedwa ake, ndiwo zikwi makumi asanu mphambu zisanu ndi ziwiri kudza mazana anai.
Iwo ndiwo mabanja a Zebuloni monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi limodzi mphambu mazana asanu.