Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.
Numeri 1:27 - Buku Lopatulika owerengedwa ao a fuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 owerengedwa ao a fuko la Yuda, ndiwo zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zinai kudza mazana asanu ndi limodzi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ataŵerenga maina onse a m'fuko la Yuda, adapezeka kuti ali 74,600. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chiwerengero cha anthu ochokera mʼfuko la Yuda chinali 74, 600. |
Ndipo Yowabu anapereka kwa mfumu kuchuluka kwa anthu adawawerenga; ndipo mu Israele munali anthu zikwi mazana asanu ndi atatu, ngwazi zosolola lupanga; ndi anthu a Yuda ndiwo zikwi mazana asanu.
A ana a Yuda, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
A ana a Isakara, kubadwa kwao, monga mwa mabanja ao, monga mwa nyumba za makolo ao, powerenga maina, kuyambira a zaka makumi awiri ndi mphambu, onse akutulukira kunkhondo;
Iwo ndiwo mabanja a Yuda monga mwa owerengedwa ao, zikwi makumi asanu ndi awiri mphambu zisanu ndi chimodzi kudza mazana asanu.