Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Nehemiya 8:5 - Buku Lopatulika

Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Ezara anafunyulula bukulo pamaso pa anthu onse, popeza iye anasomphokera anthu onse; ndipo polifunyulula anthu onse ananyamuka.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono ataimirira pansanjapo, Ezara adafutukula buku, anthu onse akupenya. Pomwepo anthu onse adaimirira.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Tsono Ezara anatsekula buku, akuona popeza anayima pa nsanja. Pamene anafutukula bukulo anthu onse anayimirira.

Onani mutuwo



Nehemiya 8:5
6 Mawu Ofanana  

Pamenepo Solomoni anati, Yehova ananena kuti adzakhala m'mdima waukulu.


Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yake, nidalitsa msonkhano wonse wa Israele. Ndi msonkhano wonse wa Israele unaimirira.


Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo.


Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.


Ndipo Ehudi anamdzera alikukhala pa yekha m'chipinda chosanja chopitidwa mphepo. Nati Ehudi, Ndili nao mau a Mulungu akukuuzani. Nauka iye pa mpando wake.