Nehemiya 8:3 - Buku Lopatulika3 Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Nawerenga m'menemo pa khwalala lili ku Chipata cha Madzi kuyambira mbandakucha kufikira msana, pamaso pa amuna ndi akazi, ndi iwo okhoza kuzindikira; ndi anthu onse anatcherera khutu buku la chilamulo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Tsono Ezara adaŵerenga bukulo atayang'ana bwalo la Chipata cha Madzi, kuyambira m'mamaŵa mpaka pa masana, pamaso pa amuna ndi akazi omwe, ndiponso onse amene ankatha kumvetsa zinthu bwino. Ndipo anthu onsewo ankatchera makutu kuti amve zoŵerengazo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Choncho Ezara anawerenga bukulo atayangʼana bwalo la Chipata cha Madzi kuyambira mmawa mpaka masana pamaso pa amuna, akazi ndi onse amene ankamvetsa bwino zinthu. Ndipo anthu onse anatchera khutu kuti amve malamulowo. Onani mutuwo |
Ndipo Ezara mlembi anaima pa chiunda cha mitengo adachimangira msonkhanowo; ndi pambali pake padaima Matitiya, ndi Sema, ndi Anaya, ndi Uriya, ndi Hilikiya, ndi Maaseiya, kudzanja lamanja lake; ndi kudzanja lamanzere Pedaya, ndi Misaele, ndi Malikiya, ndi Hasumu, ndi Hasibadana, Zekariya, ndi Mesulamu.