Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
Nehemiya 4:3 - Buku Lopatulika Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Tobiya Mwamoni anali naye, nati, Chinkana ichi achimanga, ikakwerako nkhandwe, idzagamula linga lao lamiyala. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tobiya Mwamoni amene anali naye adati, “Inde, chimene akumangacho, ngati nkhandwe ikwerapo, idzagwetseratu khoma la miyala laolo.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tobiya wa ku Amoni, amene anali naye anati, “Chimene akumangacho ngati nkhandwe itakwerapo, itha kugwetsa khoma lawolo!” |
Ndipo Benihadadi anatuma kwa iye, nati, Milungu indilange, nionjezepo, ngati fumbi la Samariya lidzafikira kudzaza manja a anthu onse akutsata mapazi anga.
Nati iye, Chinkana atulukira mumtendere, agwireni amoyo; chinkana atulukira m'nkhondo, agwireni, amoyo.
Mukokerane tsono ndi mbuye wanga mfumu ya Asiriya, ndipo ndidzakupatsani akavalo zikwi ziwiri, mukakhoza inu kuonetsa apakavalo.
Atamva Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapoloyo Mwamoni, chidawaipira kwakukulu, kuti wadza munthu kuwafunira ana a Israele chokoma.
Koma Sanibalati Muhoroni, ndi Tobiya kapolo Mwamoniyo, ndi Gesemu Mwarabu, anamva natiseka pwepwete, natipeputsa, nati, Chiyani ichi muchichita? Mulikupandukira mfumu kodi?
Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata);
Mwamoni kapena Mmowabu asalowe m'msonkhano wa Yehova; ngakhale mbadwo wao wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova, ku nthawi zonse;