Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;
Nehemiya 2:7 - Buku Lopatulika Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse makalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndinanenanso kwa mfumu, Chikakomera mfumu, indipatse akalata kwa ziwanga za tsidya lija la mtsinje, andilole ndipitirire mpaka ndifikira ku Yuda; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ndidauza mfumu kuti, “Ngati chingakukondweretseni amfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudzera m'chigawocho mpaka ndikafike ku Yuda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ndinatinso kwa mfumu, “Ngati zikondweretse mfumu, mundipatse makalata oti ndikapereke kwa abwanamkubwa a ku chigawo cha Patsidya pa Yufurate, kuti akandilole kudutsa mwamtendere mpaka nditakafika ku Yuda. |
Tsono iwe, Tatenai, kazembe wa tsidya lija la mtsinjewo, Setari-Bozenai, ndi anzanu Afarisikai, okhala tsidya lija la mtsinje, muzikhala kutali;
Ndipo ine Arita-kisereksesi, mfumu ine, ndilamulira osunga chuma onse okhala tsidya lija la mtsinjewo, kuti chilichonse akupemphani Ezara wansembe, mlembi wa lamulo la Mulungu wa Kumwamba, chichitike mofulumira;
Pakuti ndinachita manyazi kupempha kwa mfumu gulu la asilikali, ndi apakavalo, kutithandiza pa adani panjira; popeza tidalankhula ndi mfumu kuti, Dzanja la Mulungu wathu likhalira mokoma onse akumfuna; koma mphamvu yake ndi mkwiyo wake zitsutsana nao onse akumsiya.
Ndipo napereka malamulo a mfumu kwa akazembe a mfumu, ndi kwa ziwanga, tsidya lino la mtsinjewo; ndipo iwo anathandiza anthu ndi nyumba ya Mulungu.
Ndinafika tsono kwa ziwanga za tsidya lino la mtsinje, ndipo ndinawapatsa makalata a mfumu. Koma mfumu idatumiza apite nane akazembe a nkhondo, ndi apakavalo.
Ndi pambali pao anakonza Melatiya Mgibeoni, ndi Yadoni Mmeronoti, ndi amuna a ku Gibiyoni, ndi a ku Mizipa, wa ulamuliro wa chiwanga tsidya lino la mtsinje.