Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,
Mateyu 3:5 - Buku Lopatulika Pamenepo panamtulukira iye a ku Yerusalemu, ndi Yudeya yense, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo panamtulukira iye a ku Yerusalemu, ndi Yudeya lonse, ndi dziko lonse loyandikana ndi Yordani; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ochokera ku Yerusalemu ndi ku dera lonse la Yudeya, ndi ku madera onse a pafupi ndi mtsinje wa Yordani ankadza kwa iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Anthu ankapita kwa iye kuchokera ku Yerusalemu ndi ku Yudeya konse ndi ku madera onse a Yorodani. |
Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,
Ndipo inamtsata mipingomipingo ya anthu ochokera ku Galileya, ndi ku Dekapoli ndi ku Yerusalemu, ndi ku Yudeya, ndi ku tsidya lija la Yordani.
Ndipo anatuluka a ku dziko lonse la Yudeya, ndi a ku Yerusalemu onse; nadza kwa iye nabatizidwa ndi iye mumtsinje Yordani, powulula machimo ao.
Chilamulo ndi aneneri analipo kufikira pa Yohane; kuyambira pamenepo ulalikidwa Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo munthu aliyense akangamira kulowamo.
Ndipo iye anadza kudziko lonse la m'mbali mwa Yordani, nalalikira ubatizo wa kulapa mtima kuloza ku chikhululukiro cha machimo;
Chifukwa chake iye ananena kwa makamuwo a anthu amene anatulukira kukabatizidwa ndi iye, Obadwa a njoka inu, anakulangizani inu ndani kuthawa mkwiyo ulinkudza?
Ndipo Yohane analinkubatiza mu Ainoni pafupi pa Salimu, chifukwa panali madzi ambiri pamenepo; ndipo analinkufikako anthu, nalinkubatizidwa.
Iyeyo anali nyali yoyaka ndi yowala; ndipo inu munafuna kukondwera m'kuunika kwake kanthawi.