Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;
Mateyu 26:57 - Buku Lopatulika Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo iwo akugwira Yesu ananka naye kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene adasonkhana alembi ndi akulu omwe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono anthu amene adagwira Yesu aja adapita naye kunyumba kwa Kayafa, mkulu wa ansembe onse. Kumeneko kudaasonkhana aphunzitsi a Malamulo ndi akulu a Ayuda. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo amene anamugwira Yesu anamutengera kwa Kayafa, mkulu wa ansembe, kumene aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anasonkhana. |
Pomwepo anasonkhana ansembe aakulu, ndi akulu a anthu, kubwalo la mkulu wa ansembe, dzina lake Kayafa;
Koma wina mmodzi wa mwa iwo, Kayafa, wokhala mkulu wa ansembe chaka chomwecho anati kwa iwo, Simudziwa kanthu konse inu,