Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;
Mateyu 22:2 - Buku Lopatulika Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ufumu wa Kumwamba ufanafana ndi munthu, mfumu, amene anakonzera mwana wake phwando la ukwati, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Za Ufumu wakumwamba tingazifanizire motere: Mfumu ina idaakonzera mwana wake phwando laukwati. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna. |
Fanizo lina Iye anawafotokozera iwo, nanena, Ufumu wa Kumwamba ufanizidwa ndi munthu, amene anafesa mbeu zabwino m'munda mwake;
ndipo inu nokha khalani ofanana ndi anthu oyembekezera mbuye wao, pamene ati abwera kuchokera kuukwati; kuti pakudza iye, nakagogoda, akamtsegulire pomwepo.
Pakuti ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Khristu.
Ndipo muchite monga momwe ananena mau akufotokozeraniwo, ku malo amene Yehova adzawasankha; nimusamalire kuchita monga mwa zonse akulangizanizi.