Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
Mateyu 16:9 - Buku Lopatulika Kodi chikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi madengu angati munawatola? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Kodi chikhalire simudziwa, ndipo simukumbukira mikate isanu ija ya anthu aja zikwi zisanu, ndi madengu angati munawatola? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kodi mpaka pano simunamvetsebe? Kodi simukukumbukira kuti ndi buledi msanu ndidadyetsa anthu zikwi zisanu? Nanga mudaadzaza madengu angati ndi zotsala? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kodi inu simukumvetsetsabe? Kodi simukukumbukira za buledi musanu amene anadya anthu 5,000 ndi madengu amene munadzaza? |
Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;
Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.