Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.
Mateyu 13:16 - Buku Lopatulika Koma maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma maso anu ali odala, chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa “Koma inu ndinu odala, popeza kuti maso anu akupenya, ndipo makutu anu akumva. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva. |
Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.
Yesu ananena kwa iye, Chifukwa wandiona Ine, wakhulupirira; odala iwo akukhulupirira, angakhale sanaone.
kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.
Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m'mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziwitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Khristu.