Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli. Ndinazunza moyo wanga ndi kusala; ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa.
Mateyu 10:13 - Buku Lopatulika Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngati nyumbayo ili yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siili yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono ngati anthu am'nyumbamo akulandiranidi, mtendere wanuwo ukhale nawo ndithu. Koma ngati anthu am'nyumbamo akana kukulandirani, mtendere wanuwo ubwerere kwa inu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. |
Koma ine, pakudwala iwowa, chovala changa ndi chiguduli. Ndinazunza moyo wanga ndi kusala; ndipo pemphero langa linabwera kuchifuwa changa.
Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu.
Ndipo mukakhala mwana wa mtendere m'menemo, mtendere wanu udzapumula pa iye; koma ngati mulibe, udzabwerera kwa inu.