Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.
Ndipo Hezekiya anagona ndi makolo ake, namuika polowerera kumanda a ana a Davide; ndi Ayuda onse ndi okhala mu Yerusalemu anamchitira ulemu pa imfa yake. Ndipo Manase mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.