Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 13:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo iye anafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe, nati, Guwa la nsembe, guwa la nsembe, atero Yehova, Taona mwana adzabadwa m'nyumba ya Davide, dzina lake ndi Yosiya, adzaphera pa iwe ngati nsembe anthu ansembe a misanje, amene alikufukiza zonunkhira pa iwe, nadzatentha pa iwe mafupa a anthu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Ndipo mneneriyo adatemberera guwalo potsata mau a Chauta nati, “Guwa iwe, guwa iwe, imva mau a Chauta, akunena kuti, ‘Mwana wamwamuna adzabadwa pa banja la Davide, dzina lake Yosiya. Pa iwe iyeyo adzaperekapo ngati nsembe ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene amafukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mneneriyo anatemberera guwalo mofuwula potsata mawu a Yehova nati: “Guwa iwe, guwa iwe! Yehova akuti, ‘Taonani mʼbanja la Davide mudzabadwa mwana dzina lake Yosiya. Pa iwe, iyeyo adzaperekapo ngati nsembe, ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene tsopano akufukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 13:2
19 Mawu Ofanana  

Popeza mau aja anawafuula mwa mau a Yehova kutemberera guwa la nsembe la ku Betele, ndi kutemberera nyumba zonse za misanje ili m'mizinda ya ku Samariya, adzachitika ndithu.


Yosiya ndiye wa zaka zisanu ndi zitatu polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka makumi atatu mphambu chimodzi.


Pakuti atakhala mfumu zaka zisanu ndi ziwiri akali mnyamata, anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.


Imvani, miyamba inu, tchera makutu, iwe dziko lapansi, chifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.


Taona, zinthu zakale zaoneka, ndipo zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.


ndilalikira za chimaliziro kuyambira pachiyambi, ndi kuyambira nthawi zakale ndinena zinthu zimene zisanachitidwe; ndi kunena, Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse;


Fuula zolimba, usalekerere, kweza mau ako ngati lipenga, ndi kuwafotokozera anthu anga cholakwa chao, ndi banja la Yakobo machimo ao.


amene anamdzera mau a Yehova masiku a Yosiya mwana wake wa Amoni, mfumu ya Ayuda chaka chakhumi ndi chitatu cha ufumu wake.


Iwe dziko, dziko, dziko lapansi, tamvera mau a Yehova.


Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, unenere kwa mapiri a Israele, uziti, Mapiri a Israele inu, imvani mau a Yehova.


chifukwa chake, mapiri inu a Israele, imvani mau a Ambuye Yehova. Atero Ambuye Yehova kunena ndi mapiri, ndi zitunda, ndi mitsinje, ndi zigwa, ndi zipululu zopasuka, ndi mizinda yamabwinja, imene yakhala chakudya ndi choseketsa amitundu otsala akuzungulira;


ndipo ndidzakutembenuza ndi kukowa m'chibwano mwako ndi zokowera, ndi kukutulutsa ndi nkhondo yako yonse, akavalo ndi apakavalo ovala mokwanira onsewo, msonkhano waukulu ndi zikopa zotchinjiriza, onsewo ogwira bwino malupanga;


Ndipo anayankha nati, Ndinena ndi inu, ngati awa khala chete miyala idzafuula.


Kumwamba kutchere khutu, ndipo ndidzanena; ndi dziko lapansi limve mau a m'kamwa mwanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa