Marko 5:4 - Buku Lopatulika pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 pakuti ankamangidwa kawirikawiri ndi matangadza ndi maunyolo, ndipo anamwetula maunyolo, naduladula matangadza; ndipo palibe munthu anali ndi mphamvu yakumfuya. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Kale anthu adaayesa kangapo kummanga miyendo ndi zitsulo, ndiponso kummanga manja ndi maunyolo, koma iye ankangoŵamwetsula maunyolowo, ndipo zitsulo zomanga miyendozo ankangozithyola. Padaalibe ndi mmodzi yemwe wotha kumgonjetsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. |
amene anayesa nyumba yake kumanda; ndipo palibe munthu anakhoza kummanganso, inde ngakhale ndi unyolo;
Ndipo masiku onse, usiku ndi usana, anakhala m'manda ndi m'mapiri, nafuula, nadzitematema ndi miyala.
Pakuti Iye adalamula mzimu wonyansa utuluke mwa munthuyo. Pakuti nthawi zambiri unamgwira; ndipo anthu anammanga ndi maunyolo ndi matangadza kumsungira; ndipo anamwetula zomangirazo, nathawitsidwa ndi chiwandacho kumapululu.