Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Marko 2:9 - Buku Lopatulika Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chapafupi nchiti, kuuza wodwala manjenje kuti, Machimo ako akhululukidwa; kapena kuti, Nyamuka, senza mphasa yako, nuyende? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Chapafupi koposa nchiti, kumuuza wa ziwalo zakufayu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, nyamula machira ako, yamba kuyenda?’ Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ |
Ndipo mbiri yake inabuka ku Siriya konse: ndipo anatengera kwa Iye onse akudwala, ogwidwa ndi nthenda ndi mazunzo a mitundumitundu, ndi ogwidwa ndi ziwanda, ndi akhunyu, ndi amanjenje; ndipo Iye anawachiritsa.
Ndipo onani, anabwera naye kwa Iye munthu wamanjenje, wakugona pamphasa: ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao, anati kwa wodwalayo, Limba mtima, mwana, machimo ako akhululukidwa.
Pakuti chapafupi nchiti, kunena, Machimo ako akhululukidwa; kapena kunena, Tanyamuka. Nuyende?
Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali mwini ulamuliro wakukhululukira machimo padziko lapansi (ananena ndi wodwala manjenje),
Ndipo pomwepo Yesu pozindikira mumtima mwake kuti alikuganizira chomwecho mwa iwo okha, ananena nao, Muganiza bwanji zinthu izi m'mitima yanu?