Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.
Marko 2:6 - Buku Lopatulika Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao, Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma anakhalapo ena a alembi akuganizira mumtima mwao, Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma pamenepo panalinso aphunzitsi ena a Malamulo a Mose. Iwowo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, |
Ndipo Yesu pakuona chikhulupiriro chao ananena ndi wodwala manjenje, Mwana, machimo ako akhululukidwa.
Munthu amene atero bwanji? Achita mwano; akhoza ndani kukhululukira machimo, koma mmodzi, ndiye Mulungu?
Ndipo Yesu pamene anazindikira, ananena nao, Bwanji mutsutsana chifukwa mulibe mkate? Kodi kufikira tsopano simuzindikira, nisimudziwitsa? Kodi muli nayo mitima yanu youma?
ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;