chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa.
Luka 7:8 - Buku Lopatulika Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pakuti inenso ndili munthu wakumvera akulu anga, ndili nao asilikali akumvera ine: ndipo ndinena kwa uyu, Muka, namuka; ndi kwa wina, Idza, nadza; ndipo kwa kapolo wanga Tachita ichi, nachita. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inetu ndili ndi akuluakulu ondilamulira, komanso ndili ndi asilikali amene ineyo ndimaŵalamulira. Ndimati ndikauza wina kuti, ‘Pita’, amapitadi. Ndikauzanso wina kuti, ‘Bwera’, amabweradi. Ndipo ndikauza kapolo wanga kuti, ‘Chita chakuti’, amachitadi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pakuti ndili pansi paulamuliro, ndiponso ndili ndi asilikali pansi panga. Ndikamuwuza uyu kuti, ‘Pita,’ iye amapita; ndi uyo kuti, ‘Bwera,’ amabwera. Ndikamuwuza wantchito wanga kuti, ‘Chita ichi,’ amachita.” |
chifukwa chake ine sindinadziyesera ndekha woyenera kudza kwa Inu: koma nenani mau, ndipo mnyamata wanga adzachiritsidwa.
Koma Yesu pakumva zimenezo anazizwa naye, napotolokera kwa anthu a mpingo wakumtsata Iye, nati, Ndinena kwa inu, sindinapeze, ngakhale mwa Israele, chikhulupiriro chachikulu chotere.
Ndipo Paulo anadziitanira kenturiyo wina, nati, Pita naye mnyamata uyu kwa kapitao wamkulu; pakuti ali nako kanthu kakumfotokozera iye.
Ndipo anaitana akenturiyo awiri, nati, Mukonzeretu asilikali mazana awiri, apite kufikira Kesareya, ndi apakavalo makumi asanu ndi awiri, ndi anthungo mazana awiri, achoke ora lachitatu la usiku;
Pamenepo ndipo asilikali, monga adawalamulira, anatenga Paulo, napita naye usiku ku Antipatri.
Ndipo analamulira kenturiyo amsunge iye, koma akhale nao ufulu, ndipo asaletse anthu ake kumtumikira.
Koma ndilibe ine kanthu koti ndinenetse za iye kakulembera kwa mbuye wanga. Chifukwa chake ndamtulutsira kwa inu, ndipo makamaka kwa inu, Mfumu Agripa, kuti, ndikatha kumfunsafunsa, ndikhale nako kanthu kakulembera.
Akapolo inu, mverani m'zonse iwo amene ali ambuye monga mwa thupi, wosati ukapolo wa pamaso, monga okondweretsa anthu, komatu ndi mtima wakulinga kumodzi, akuopa Ambuye;