Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu.
Luka 7:1 - Buku Lopatulika Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m'makutu a anthu, analowa mu Kapernao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Yesu adamaliza mau ake onse m'makutu a anthu, analowa m'Kapernao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Yesu atatsiriza kulankhula zonsezi ndi anthu aja, adapita ku Kapernao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yesu atamaliza kunena zonsezi pamaso pa anthu amene ankamvetsera, analowa mu Kaperenawo. |