Luka 6:49 - Buku Lopatulika49 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201449 Koma iye amene akumva, ndi kusachita, afanafana ndi munthu wakumanga nyumba pa nthaka yopanda maziko; pa imeneyo unagunda mtsinje, ndipo inagwa pomwepo; ndipo kugumuka kwake kwa nyumbayo kunali kwakukulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa49 Koma munthu wongomva mau anga, osaŵagwiritsa ntchito, amafanafana ndi munthu amene adaamanga nyumba pamwamba pa nthaka, osakumba maziko. Pamene madzi a chigumula adagunda nyumbayo, pompo idagwa, ndipo kuwonongeka kwake kunali kotheratu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero49 Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.” Onani mutuwo |