Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.
Luka 5:4 - Buku Lopatulika Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene Iye analeka kulankhula, anati kwa Simoni, Kankhira kwa kuya, nimuponye makoka anu kukasodza. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatsiriza kulankhula, adauza Simoni kuti, “Sunthirani kozamako, muponye makoka anu kuti muphe nsomba.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.” |
Koma kuti ife tisawakhumudwitse, pita iwe kunyanja, ukaponye mbedza, nuitole nsomba yoyamba kuwedza; ndipo ukaikanula pakamwa pake udzapezamo rupiya; tatenga limeneli, nuwapatse ilo pamutu pa iwe ndi Ine.
Ndipo Simoni anayankha, nati, Ambuye, tinagwiritsa ntchito usiku wonse osakola kanthu, koma pa mau anu ndidzaponya makoka.
Koma anati kwa iwo, Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza. Pamenepo anaponya, ndipo analibenso mphamvu yakulikoka chifukwa cha kuchuluka nsomba.