Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Luka 1:57 - Buku Lopatulika Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo inakwanira nthawi ya Elizabeti, ya kubala kwake, ndipo anabala mwana wamwamuna. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Nthaŵi yakuti Elizabeti achire idakwana, ndipo adabala mwana wamwamuna. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Itakwana nthawi yoti Elizabeti abereke, anabereka mwana wamwamuna. |
Mulungu sindiye munthu, kuti aname; kapena mwana wa munthu, kuti aleke; kodi anena, osachita?
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.
Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti.
Ndipo anansi ake ndi abale ake anamva kuti Ambuye anakulitsa chifundo chake pa iye; nakondwera naye pamodzi.