Luka 1:5 - Buku Lopatulika Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana aakazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Masiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali munthu wansembe, dzina lake Zekariya, wa gulu la ansembe la Abiya; ndi mkazi wake wa ana akazi a fuko la Aroni, dzina lake Elizabeti. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pa nthaŵi imene Herode anali mfumu ya dziko la Yudeya, kunali wansembe wina, dzina lake Zakariya, wa gulu la ansembe la Abiya. Mkazi wake Elizabeti anali wa fuko la Aroni. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mʼmasiku a Herode, mfumu ya Yudeya, kunali wansembe dzina lake Zakariya wa gulu la ansembe la Abiya; mkazi wake Elizabeti analinso wa fuko la Aaroni. |
Awa ndi malongosoledwe ao mu utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.
Ndipo pa kubadwa kwake kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya m'masiku a Herode mfumu, onani, Anzeru a kum'mawa anafika ku Yerusalemu,
Koma mngelo anati kwa iye, Usaope Zekariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako Elizabeti adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.