ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;
Hoseya 3:3 - Buku Lopatulika ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo ndinati kwa iye, Uzikhala ndi ine masiku ambiri, usachita chigololo, usakhala mkazi wa mwamuna aliyense; momwemo inenso nawe. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndidamuuza mkaziyo kuti, “Uzikhala nane masiku ambiri, osachitanso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina. Nanenso ndidzachita chimodzimodzi.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, “Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe.” |
ungachite pangano ndi iwo okhala m'dzikomo; ndipo angachite chigololo pakutsata milungu yao, nangaphere nsembe milungu yao, ndipo angakuitane wina, nukadye naye nsembe zake;
navule zovala za ukapolo wake, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wake, ndi mai wake mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wake, ndi iye akhale mkazi wanu.