Genesis 8:11 - Buku Lopatulika ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa padziko lapansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 ndipo njiwa inadza kwa iye madzulo; ndipo, taonani, m'kamwa mwake munali tsamba la azitona lothyoledwa: ndipo anadziwa Nowa kuti madzi analimkuphwa pa dziko lapansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Madzulo idabwerako, ndipo Nowa adaona kuti kukamwa kwake kuli tsamba laliŵisi la mtengo wa olivi. Apo Nowa adadziŵa kuti madzi ayamba kuphwa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. |
Ndipo analindanso masiku ena asanu ndi awiri; natulutsa njiwayo: ndipo siinabwerenso konse kwa iye.
ndi kuti azilalikira ndi kumveketsa m'midzi mwao monse ndi mu Yerusalemu, ndi kuti, Muzitulukira kuphiri, ndi kutengako nthambi za azitona, ndi nthambi za mitengo yamafuta, ndi nthambi za mitengo yamchisu, ndi zinkhwamba za migwalangwa, ndi nthambi za mitengo zothonana, kumanga nazo misasa monga munalembedwa.
Ndipo adzalalikira bwanji, ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.