Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Genesis 41:7 - Buku Lopatulika Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo ngala zoondazo zinameza ngala zisanu ndi ziwiri zonenepa ndi zodzalazo. Ndipo Farao anauka, ndipo, taonani, analota. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ngala zofwapazo zidameza ngala zisanu ndi ziŵiri zokhwima zija. Farao atadzuka, adaona kuti anali maloto chabe. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ngala zowonda zija zinameza ngala zathanzi ndi zonenepa zija. Farao anadzidzimuka ndipo anaona kuti anali maloto chabe. |
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Ndipo, taonani, ngala zisanu ndi ziwiri, zoonda zopserera ndi mphepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pao.
Ndipo panali m'mamawa mtima wake unavutidwa; ndipo anatumiza naitana amatsenga onse a mu Ejipito, ndi anzeru onse a momwemo: ndipo Farao anafotokozera iwo loto lake; koma panalibe mmodzi anakhoza kuwamasulira iwo kwa Farao.
Ndipo Solomoni anauka, ndipo taona, ndilo loto; nabwera ku Yerusalemu, naima ku likasa la chipangano cha Yehova, napereka nsembe zopsereza ndi nsembe zamtendere, nakonzera anyamata ake onse madyerero.