chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.
Genesis 40:16 - Buku Lopatulika Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamutu panga; Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene wophika mkate anaona kuti kumasulira kwake kunali kwabwino, iye anati kwa Yosefe, Inenso ndinalimkulota, ndipo, taonani, malichero atatu a mikate yoyera anali pamtu panga; Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Wophika buledi uja nayenso adaona kuti tanthauzo la malotowo linali labwino, adauza Yosefe kuti, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi pamutu pangapa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkulu wa opanga buledi ataona kuti Yosefe wapereka tanthauzo labwino, anati kwa Yosefe, “Inenso ndinalota nditasenza nsengwa zitatu za buledi. |
chifukwa kuti ndinabedwa ndithu m'dziko la Ahebri; ndiponso pano sindinachite kanthu kakundiikira ine m'dzenjemu.
m'lichero lapamwamba munali mikate ya Farao ya mitundumitundu; ndipo mbalame zinadya ya m'lichero la pamutu panga.